Ndaipa Lero
Billy Kaunda
Mimba yake bambo ake anayika Sindifunaso mwana ine uyu yekha mukachotsetse Mayi wake ndi chikondi nakakakamira Mpaka banja linatha anabadwa mkukula movutikira Mpaka tsiku lina mwana atafooka ndi njala Adakaba ku maliro, nsima ndi ndiwo Mpaka tsiku lina mwana fees itasowa Adapita pa hotel uhule mwana aphunzire Oooh why? Akanadziwa mayi mayiyo Mwana ali m'mimbayo akadzabadwa Adzawanyoza, adzawakana akanamutani? Akanadziwa nzakeyo Bwezi ndikuthandiza zikayenda Adzamutaya, adzamunyoza akanamutani? Chosadziwa, chosadziwa Chosadziwa, zimangochitika Namalenga, amaona Ndalakwanji? zimangochitika Oooh why? Waphunzira mkumaliza lero walemera Wayambapo kunyoza mayi mumkaba komanso uhule Akabwera ku town akumawazemba Dziko likudabwa ndiwe munthu wanji Kodi wayiwala? Ulavure nsimayo poti inali yakuba Ung'ambe degree poti fees ya uhule Waliputa tsoka ona njala yavuta Chaka ndiye chatha popanda chochita Oooh why? Eh yeah, eh yeah, eh yeah Akanadziwa mayi mayiyo Mwana ali m'mimbayo akadzabadwa Adzawanyoza, adzawakana akanamutani? Akanadziwa nzakeyo Bwezi akuthandiza zikayenda Adzamutaya, adzamunyoza akanamutani? Chosadziwa, chosadziwa Chosadziwa, zimangochitika Namalenga, amaona Talakwanji? mukhululuke Kundidabwitsa dyamani anthu amakono Kutembenuka poyela kutukwana mayi kufuna mipando Amkaphuzitsa ku Madalasi ku Mpemba Anali ma nobody awatsukatsuka kumalalata Zoonadi ndalama inapha Yesu Ndimadina dance Ma phwando a wisiki Mudzatikumbukira kunja kukacha Tinkakoma mu dzinja, mchilimwe tanyasa Yeah hii why? Akanadziwa mayi mayiyo Mwana ali m'mimbamu akadzabadwa Adzawanyoza, adzawakana akanamutani? Akanadziwa nzakeyo Bwezi ndikuthandiza zikayenda Adzamutaya, adzamunyoza akanamutani? Chosadziwa, chosadziwa Chosadziwa, zimangochitika Namalenga, amaona Talakwanji? mukhululuke Oooh why? Chosadziwa, chosadziwa Chosadziwa, zimangochitika Namalenga, amaona (talakwanji? mukhululuke)