Mzimu Wa Soldier
Lucius Banda
5:18Khalani khala oh, osangalala Zosowa zanga Mbuye mumandipatsa Koma chimodzi chomwe chimandivuta oh Ndimawasowa mayi wanga Ndimakhumbira mayi wanga Mkajomba kumunda mayi Kundimana nsima Mkathawa sukulu mayi kundikwapula Ndimkangoti nkhanza mayi Ine chibwana aa aa! Chinali chikondi mama inu Ndimakhumbira mayi wanga Lero ndikulira (mayi wa weh) Amayi wanga Analowa mmanda asanadyelele Anzathu alinawo mayi wo timawasilira Akamawapatsa chitenje Timasilira mama ine Chauta kumwamba oh mundisamalire Amayi ndi mayi aposa zonse Inu muli nawo amoyo muwasamalire Timasilira mama ife Timasilira mama ife Ndikamakumbuka oh zophika zawo Kholowa, bonongwe mama maka chisoso Akati achape mama ngati wamira mayi Ndimawasowa mayi wanga Ndimakhumbira mayi wanga Tisamanamizane anzanga kuti umasiye Ndi umphawi okha, usiwa kapena njala Ungapeze zonse chuma banja mkutchuka Udzawasowa mayi wako Ndimasilira mayi ine Lero ndikulira (mayi wa weh) Amayi wanga Analowa mmanda asanadyelele Anzathu alinawo mayi wo timawasilira Akamawapatsa chitenje Timasilira mama ine Chauta kumwamba oh mundisamalire Amayi ndi mayi aposa zonse Inu muli nawo amoyo muwasamalire Timasilira mama ife Timasilira mama ife Lero ndikulira (mayi wa weh) Amayi wanga Analowa mmanda asanadyelele Anzathu alinawo mayi wo timawasilira Akamawapatsa chitenje Timasilira mama ine Chauta kumwamba oh mundisamalire Amayi ndi mayi aposa zonse Inu muli nawo amoyo muwasamalire Timasilira mama ife (masiku onse mama) Timasilira mama ife (helele oh mother's day) Achikhala ali moyo (timasilira mama ife) Akanaphika thowa (timasilira mama ife) Dzidzukulu mkumamwa (timasilira mama ife) Oh mother's day (timasilira mama ife) Pa ukwati wanga (timasilira mama ife) Ooh yah Ambuye muwapatse anthu akufa Chiuziro chosatha Muwalitse nyumba zawo Awuse ndi mtendere Awuse mu mtendere Amen! Amama amama amama Amama amama amama Ooh amawo amawo amawo Amen! Amama amama amama Amama amama amama Ooh amawo amawo amawo Ah amawo amawo amawo