Ndaipa Lero
Billy Kaunda
Kodi ndi angati akukondwa? Kodi ndi angati akulira? Cheteyutu ndi mantha M'mitima muli zinkhani Nzeru zayekha adanyika Abale muti amava za anzanu? Olo tinyozeke bwanji Nafe Malawi ndi kwathu Muja adayimbila Galatiya Tayamba bwino kumaliza mwachithaya Mudali bwenzi lathu ambiri Agalu okuwakuwa tidali ochepa Mwa luso lanu mudatimanga pa chain Agalu tonse tidakhala chete Pomwe kumacha panyumba paja pabedwa Ufulu ndi chuma tangotsala ndi ufa Abale munthu samayipa zonse Pali zambiri zofunika mapanga Tikuyamika zitukuko zambiri Zimene mwayesetsa kutipangira Mwamanga zambiri makamaka misewu Mwathetsa njala ndipo anthu tawona Koma abwana chikuvuta ndichani? Zoyipa zayamba kufufuta zabwino Kodi ndi angati akukondwa? Kodi ndi angati akulira? Cheteyutu ndi mantha Mu mtima muli zinkhani Nzeru zayekha adanyika Abale muti amava za anzanu? Olo tinyozeke bwanji ife Nafe Malawi ndi kwathu Tikamalira mudzitimvera Timati inu m'bambo athu Tikayimba musamakwiye Timafuna mumve malango Tikamalira mudzitimvera Timati inu m'bambo athu Tikayimba musamabane Mudzingomvapo langizolo Ay yeah yeah yeah yeah Ay yah yah yah yah Ay yeah yeah yeah yeah Mayo mayo Mmh Wobeleka sake ndathu ena Poti wobwezela ufikire kwa ana Abale mmafika pothamangitsa kazembe Zotsatila zidzaphinja aphawi Muli ndi zonse zosowa mkapa moyo Olo nzungu atakwiya mungathe kulimba Koma ifeyo amphawi akumudzi Timadalira thandizo la azunguwo Kumvetsa chisoni anzathu alimi Alima mbewu kusowa ogula Ogula fodya munawathamangitsa Koma zonsezi ovutika ndi ife Mitengo yafodya ya masiku ano Zomvetsa chisoni mlimi ali m'mavuto Wa business ngokondwela popereka Ma okala atilanda m'ma china Kodi ndi angati akukondwa? Kodi ndi angati akulira? Cheteyutu ndi mantha M'mitima muli zinkhani Nzeru zayekha adanyika Abale muti amava za anzanu? Olo tinyozeke bwanji ife Nafe Malawi ndi kwathu Tikamalira mudzitimvera Timati inu m'bambo athu Tikayimba musamabane Timafuna mumve malango Tikamalira mudzitimvera Timati inu m'bambo athu Tikamayimba musamatide Timangofuna muchite chilondola Ay yeah yeah yeah yeah Ay yah ooh Oooh Tililiti-titete-titili-tete Hahaha Ay yah yah Kodi ndi angati akukondwa? Kodi ndi angati akulira? Cheteyutu ndi mantha Mu mitima muli zinkhani Nzeru zayekha adanyika Abale muti amava za anzanu? Olo tinyozeke bwanji Nafe Malawi ndi kwathu Tikamalira mudzitimvera Timati inu m'bambo athu Tikayimba musamakwiye Timafuna mumve malango (Tikamalira mudzitimvera)