Ndaipa Lero
Billy Kaunda
Zakuti uyu wachoka ku Mpoto zisiyike Zakuti uyunso wachoka ku M'mwela-nso zithe Zakuti ndi Mlomwe, ndi Mchewa zichepe Tonse ndi a Malawi likakhala dziko ndi lathu Tonse ndi a Malawi, wolemera wosawuka Tisateye nthawi kukhala wokhumbana mitundu Musachedwe anzanga mkukumbana mitundu Munthu aliyense ali ndi mphatso zake Ndale zanu musamapangire pa guwa Poti tchalitchi ndi la Mbuye Mulungu Achisilamu amamutchula Allah Akatolika amamutchula Yahweh A dutch nawo amamutchula Jehovah Koma Iye ndi m'modzi Osabisala kuseli kwa mipingo Zakuti nsilamu achoke pa udindo Sizingatitchove abale musayiwale Christu pamaso kumbali mkumapha Kulibwino kukhala ndi nsilamu wachikondi Mavuto anthu ndi uphawi si mipingo Musabweze dziko m'manja mwa satana Musachedwe anzanga mkukumbana mitundu Munthu aliyense ali ndi mphatso zake Ndale zanu musamapangire pa guwa Poti tchalitchi ndi la Mbuye Mulungu Awo achisilamu amamutchula Allah Akatolika amamutchula Yahweh A dutch nawo amamutchula Jehovah Koma Iye ndi m'modzi Oh usabisala kuseli kwa mipingo Pakuti ku Mpoto kukanakhala ka dziko Bwezi dzina lakelo likanakhala ndi poto Abale Ifeyo ndi amodzi tikondane Musalore anthu andale kukunamizani Anthu akunja akalowa kumwamba Ansembe, abusa muli busy kulimbana ndi ndale Musachedwe anzanga mkukumbana mitundu Munthu aliyense ali ndi mphatso zake Ndale zanu musamapangire pa guwa Poti tchalitchi ndi la Mbuye Mulungu Achisilamu amamutchula Allah Akatolika amamutchula Yahweh A dutch nawo amamutchula Jehovah Koma Iye ndi m'modzi Oh osabisala kuseli kwa mipingo Musachedwe anzanga mkukumbana mitundu Munthu aliyense ali ndi mphatso zake Ndale zanu musamapangire pa guwa Poti tchalitchi ndi la Mbuye Mulungu Achisilamu amamutchula Allah Akatolika amamutchula Yahweh A dutch nawo amamutchula Jehovah Koma Iye ndi m'modzi Osabisala kuseli kwa mipingo Musachedwe anzanga mkukumbana mitundu Munthu aliyense ali ndi mphatso zake Ndale zanu musamapangire pa guwa Poti tchalitchi ndi la Mbuye Mulungu Awo achisilamu amamutchula Allah Akatolika amamutchula Yahweh A dutch nawo amamutchula Jehovah Koma Iye ndi m'modzi Osabisala kuseli kwa mipingo (Achisilamu amamutchula Allah) (Akatolika amamutchula Yahweh) (A dutch nawo amamutchula Jehovah)