Mundiwuze
Billy Kaunda
6:12Wandituma Chauta, wandituma Kuti mkambe nanu anthu anga Akuti za m'dziko nzachabe Ati zonse tiziona leroli Palibe chomwe ndi chachilendo Zonsezi, zinalipo kalero Kunali mafumu wolamulira Akayankhula aliyese kumvetsa Ali kuti lero? mudzifunse Kunali asungwana wokongola Kusekelera ngati asasiye Ali kuti lero? mudzifunse Kunali anyamata ovala bwino Kuvala ngati asokera pompo Ali kuti lero? mudzifunse Zachabechabe, zinthu zonsezi zachabe Atero mlaliki, ati zonsezi zachabe Zongosautsa mtima, zinthu zonsezi zachabe Tisazitsatire, poti zonsezi zachabe Ntchito za munthu zimasautsa Kodi nanga apindula chani Poti dzuwali, lingozungulirabe Mitsinje ithira madzi m'nyanja Nanga bwanji nyanja siyisefuka? Kubwelera kwachokera mtsinjewo Zinthu zonse zolemetsa mutu Sangathe kufotokoza zonse Maso sakhuta, satopa kuona Makutu sakhuta nako kumva Chomwe chinawoneka chidzawoneka Chochitika, Chidzachitikanso Za moyo uno nzachabechabe Zimasintha kukondweletsa mtima Atero mlaliki Zili chabe Zachabechabe, zinthu zonsezi zachabe Atero mlaliki, ati zonsezi zachabe Zongosautsa mtima, zinthu zonsezi zachabe Tisazitsatire, poti zonsezi zachabe Chilichonse chili ndi nthawi yache Nthawi yakubadwa ndi yakufa Yodzala, ndi ya kudzula Nthawi yakupha ndi yakuchiza Yakupasula ndi yakumanga Ya misozi ndi yakuseka Pali nthawi ya munthu yolira Ndipo pali ina yakuvina Yomwaza, ndi yotolera Msakondwe ndi nzeru ya padziko Munzeru yambiri muli chisoni, chambiriso Atero mlaliki Mowonjezera nzeru awonjezera Zowawa nzochuluka komanso Kukhala chitsiru, sikwabwininso Zachabechabe, zinthu zonsezi zachabe Atero mlaliki, ati zonsezi zachabe Zongosautsa mtima, zinthu zonsezi zachabe Tisazitsatire, poti zonsezi zachabe Zachabechabe, zinthu zonsezi zachabe Atero mlaliki, ati zonsezi zachabe Zongosautsa mtima, zinthu zonsezi zachabe Tisazitsatire, poti zonsezi zachabe